The History of the Late "Tremour" Malawian talented musical artist

 

MBIRI YOKHUDZA TREMOUR


Anabadwa pa 26 September 1996


Dzina la pa nsonkho adali Victor Mwangobola


Anabadwira ku Chipatala cha St Johns ku Mzuzu


Anali oyamba kubadwa mu banja la ana atatu


Maphunziro ake sadayambire mu kalasi ya Nursery ayi, iye adayambira primary kalasi ya 1 ndi 2 pa St Peters Primary School ku Mzuzu


Atalemba mayeso ake a standard 8 (PLSCE) adasankhidwira ku Katoto Secondary School. 


Pa Katoto Secondary school ndi pomwe adalembera mayeso ake a MSCE mu chaka cha 2015


Mu 2017 adayamba maphunziro a utolankhani (Journalism and Media Studies) pa sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe Technical


Kamba ka mavuto a za chuma adaphunzirako semister imodzi yokha. 


Iye adayamba bizinezi ya mu Barbershop kumene amameta tsitsi. 


Kukhala oimba iye anatchuka ndi dzina la TREMOUR pamene amaimba ndi kulemba nyimbo za chamba cha Afro_Pop ndi Reggae dancehall


Tremour adatchuka kwambiri atatulutsa nyimbo yotchedwa “Mpanipani” imene imakamba zolimbikitsa anthu amene amakhala ndi chikaiko kuti atha kupambana mu moyo wawo wa tsiku ndi tsiku 


Nyimbo zake zambiri zinali za chiyankhuro cha Chichewa, English ndi kuphatikiza Chitumbuka


Tremour adamwalira pa 30 July 2023 pamene adali chipatala atavulara kwambiri pa ngozi ina imene adagundidwa ndi Galimoto pamene iye adali pa njinga ya Moto.


Rest in peace 






Post a Comment

0 Comments